Nthambi yoona za ngozi zogwa mwadzidzi ya Department of Disaster Management Affairs- Dodma yati ili tcheru powonetsetsa kuti katundu ndi miyoyo ya anthu isaonongeke ngati mvula yomwe ikugwa m’madera ena Ingachititse kusefukira kwa madzi.
Masiku apitawa nthambi yowona za nyengo m’dziko muno inalengeza kuti mvula yochuluka igwa m’madera ena a dziko lino kuphatikizapo ku Nkhotakota, ndi Salima mwa ena, sabata ino.
M’mau ake, M’neneri wa bungwe la Dodma, a Chipiliro Khamula ati Dodma yayamba kale kutumiza akatswiri opulumutsa anzawo pa ngozi zogwa mwadzidzi m’maboma omwe ali pa chiopsezo.