M’khala kale pa ndale a Patricia Kaliati achenjeza amayi omwe akupikisana nawo pa chisankho cha sabata la mawa kuti achepetse kudziyenereza kuti apambana kale chisankhochi ponena kuti kudziyenereza kumachotsa chidwi cha ovota pa chisankho.
Iwo anena izi pamene anali mulendo olemekezeka pa mkumano wa amayi omwe akuyima m’maudindo osiyanasiyana pa chisankhochi ku Wapansi Hotel m’boma la Mangochi.
Malingana ndi a Kaliati “Mukadziyenereza anthu asanakusankheni mulephera chifukwa choti nthawi ya chisankho mabwana ndi anthu ovota, apatseni ulemu ndipo adzakukondani ndikukuvoterani,” atero a Kaliati.
Iwo ati ma udindo a ndale ndi mayitanidwe ndipo alangiza amayiwa kusamala mayankhulidwe, zochitika komanso mavalidwe ponena kuti ngati m’dindo, mayi amakhala chitsanzo kwa atsikana ndi amayi achichepere.