Zina ukaona: Kamba anga Mwala

Anthu ochuluka lero, 2 April 2025, mamawa anakhamukira ku msika wa Sumbi ku Monkey Bay m’boma la Mangochi komwe amakaona mnyamata wina wa zaka za pakati pa 20 ndi 30 yemwe ali mu ululu oopsa atachita za chisembwele ndi mkazi wa mwini ku Makanjira m’boma lomweli.

Mnyamatayu yemwe timutchule kuti John Chimtengo ,lomwe si dzina lake leni-leni anauza anthu omwe amuyang’anira kuti pa 28 March chaka chino anagona ndi mkazi yemwe mwamuna wake ali mdziko la South Africa.

John akuti izi zitachitika anabwelera kwa Sumbi ali bwinobwino koma patadutsa masiku ochepa ndipamene iye anayamba kuona zizindikiro zachilendo ku malo ake obisika ndipo pofika nthawi yomwe timafika pa msika wa Sumbi pomwe m’nyamatayu amapempha thandizo kuti abwelere ku mudzi kwawo,ndikuti atavulala kwambiri ku malo ake obisika.

Mnyamatayu anatinso akafuna kutaya madzi,akumatulutsa nsomba za mtundu wa usipa m’malo mwa mkozo.

Pakadalipano anthu akufuna kwabwino amuthandiza mnyamatayu ndipo wanyamuka ulendo opita kwawo ku Phalombe.

Related posts

Andale Achimayi awapempha kuti alemekezeke Ovota

Elephant kills a Man in Kwilasya Village

Moyo ukulimba: Malipiro sakuoneka