M’modzi mwa achinyamata oyimba Chamba cha Afro Hip-Hop Ku Monkey Bay m’boma la Mangochi yemwe amadziwika ndi dzina la “SHYZEE” wamwalira m’bandakucha wa lero lolemba pa 24 March 2025 potsatira ngozi ya pa msewu ya njinga ya moto yomwe inachitika dzulo la mulungu mumsewu wa Mangochi-Monkey Bay wa M10.
Thupi la SHYZEE yemwe amakhalira kwa Sumbi likuyembekezeka kulowa m’manda lero pa 24 March 2025.