Home Featured Ntchito za Climate Just Communities Zayenda Bwino

Ntchito za Climate Just Communities Zayenda Bwino

by Peter Dziyende
0 comments

Ntchito za Climate Just Communities, akuti zayenda bwino ndipo zipindulira anthu a m’maboma okwana 7 omwe ntchitozi zimagwilidwa.

‎Polankhula pa mkumano wa mabungwe osiyanasiyana omwe amagwira ntchito mu project-yi amaunikira momwe agwilira ntchito zawo, mkulu otsogolera ntchito za project-yi a Ken Matekenya anati ndi okhutira poona kuti anthu am’madera atenga umwini pa ntchito zachitukuko zomwe zagwilidwa mmadera awo ndipo kuti tsopano anthu ali ndikutekera kulankhula ndi adindo pa nkhani zomwe anthuwa akufuna mmadera awo.

‎a Matekenya anati ngakhale kuti ntchito za project-yi zikupita kumapeto, ali ndi chikhulupiliro cholimba kuti anthu apitiliza kugwira ndi kusamalira ntchito zomwe zakhazikitsidwa ndi project-yi.

‎Mwa ntchito zina zomwe zagwilidwa mu project-yi, ndi kumanganso kwa ofesi ya aphunzitsi pa sukulu ya primary ya Ngokwe ku Machinga ndi bungwe la Organisation for Sustainable Socio-Economic Development Initiative (OSSEDI Malawi).

Ku Karonga bungwe la Cadecom lathandizira kumanga malo osamalira anthu omwe akusowa pokhala kamba ka ngozi zobwera kamba kakusintha kwa nyengo m’bomalo

Kudzanso ntchito zopeleka madzi aukhondo ku kwa anthu ku dera la TA Tombondera m’boma la Chikwawa ndi bungwe la
‎Water Witness Malawi. Kungotchulapo zochepa.

‎Ntchito za Climate Just Communities zinali za zaka zitatu kuyambira m’chaka cha 2023 ndipo zimagwilidwa ndi mabungwe osiyanasiyana m’maboma a Machinga, Neno, Chikwawa, Phalombe, Karonga, Zomba and Salima.

Omwe amatsogolera ntchitozi ndi a DAI Global UK ndi thandizo kuchokera ku Scottish Government pansi pa the Climate Justice Fund ndipo ntchito ngati zomwezi zimagwilidwa m’maiko a Zambia ndi Rwanda.

You may also like

Leave a Comment

Dzimwe Community Radio is nonprofit making institution currently located behind the Community Resource Centre Hall to the South East of Monkey Bay Airstrip. The radio was established in 1998 initially funded by UNITED NATION EDUCATION SCIENTIFIC AND CULTURE ORGANISATION (UNESCO) to act as a platform where people can discuss issues and find lasting solutions that concern them to achieve sustainable development.

Newsletter

Subscribe my Newsletter for new blog posts, tips & new photos. Let's stay updated!

@2025 – All Right Reserved. MACRA Community Radios

Are you sure want to unlock this post?
Unlock left : 0
Are you sure want to cancel subscription?
-
00:00
00:00
Update Required Flash plugin
-
00:00
00:00