Ngati njira imodzi yofuna kuchepetsa ngozi mu nseu wa Mangochi-Monkey-bay, phungu wa dera la Monkey bay, a Ralph Jooma ayamba ntchito yokonza nseu-wu yomwe ndi ya ndalama zokwana pafupifupi 2 million kwacha.
Poyankhula ndi a Jooma, iwo ati kupatula kuchititsa ngozi, kuonongeka kwa nsewu wa Mangochi-Monkeybay kwakhala kukubweretsa mavuto osiyanasiyana monga kukwera mtengo kwa maulendo a pa nseu, kubwerela m’mbuyo kwa ntchito zokopa alendo, komanso kuonongeka kwa katundu monga nsomba zisanafike pa nsika kaamba kochedwa pa nseuwu.
Iwo anati akhala akupereka madando a vuto la kuonongeka kwa nseuwu ku boma m’nyumba ya malamulo koma mpaka pano sanalandirebe yankho.
Nseuwu umalumikiza madera monga Mangochi boma, Golomoti komanso Monkey bay pa ntchito za malonda, zokopa alendo ndi zina .