Ogwira ntchito kumsika wa Monkey-Bay omwe ndi alonda komanso otolera misonkho omwe amagwira ntchito pansi pa Khonsolo ya boma la Mangochi adandaula ndikuchedwa kwa khonsoloyi kuwapatsa malipilo awo kwa miyezi isanu ndi umodzi (6) tsopano.
Mmodzi mwaokhudzidwa yemwe anapempha kuti tisamutchule dzina, wati kusalandira kwa malipiloku kwadzetsa mavuto ochuluka pamoyo wawo, kaamba koti akulephera kugula zinthu zofunikila pamoyo monga chakudya ndizina zapakhomo kuphatikizapo kulipila nyumba zomwe akukhala.
” Takhala miyezi six pano opanda malipiro. Izi zadzetsa mabvuto ochuluka pa miyoyo yathu, tikulephera kulipila rent, kugula chakudya, ngakhalenso kulipilira fizi ana athu, tikunena pano kusukulu anathamangitsidwa kalekale “. Iwo atero.
Malingana ndi iwowa, ngakhale akhala akuchita mikumano yosiyanasiyana ndi akuluakulu awo akukhonsolo pazankhaniyi omwe akhala akuwalonjeza kuti awapatsa malipirowa pakamodzi koma mpaka pano sadalandirebe ndalamazi.
“Adatilonjeza kuti atipatsa ndalama zathu zonse kumapeto amwezi wa February chaka chino koma kufikila pano mwezi wa April adangotipatsapo malipiro amwezi umodzi basi, watero mmodzi mwa ogwira ntchitowa.
Titawafunsa kuti ayikepo ndemanga pa nkhaniyi, m’neneri ku khonsolo ya boma la Mangochi a Bishop Witmos, ati khonsoloyi imakumana ndi bvuto lazachuma lomwe lidachititsa kuchedwa kwa malipilowa komabe iwo ati bvutoli lakozedwa tsopano ndipo ena mwa ogwira ntchitowa ayamba kale kulandila ndalama zawo lero pomwe ena alandila lolemba sabata lamawa.