Mkulu owona mapulani a za chitukuko ku Mangochi a Chris Nawata ati nkhani yosamba m’manja yatsamira pakusintha kaganizidwe ndipo khonsoloyi ikudalira adindo ngati mafumu, atsogoleri a mabungwe komanso zipembedzo kuti kusamba m’manja nthawi zonse kukhale chikhalidwe.
M’mawu awo a gulupu a Matuwi am’dera la Senior Chief Mponda atsindika pochenjeza anthu kuti ku nyanja sikubafa kosambira kapena kuchitira chimbudzi ndipo alimbikitsa onse kumanga zimbudzi m’makomo mwawo mvula isanayambe.
Poyikapo mulomo pa nkhaniyi, katswiri wa za ukhondo ndikusintha chikhalidwe ku bungwe la WaterAid a Maria Soko ati kusintha kaganizidwe sintchito ya tsiku limodzi ndipo mavuto a zachilengedwe ngati anamondwe komanso miliri yomwe boma la Mangochi lakumana nawo m’zaka ziwiri zapitazi ndiomwe akokera pansi ntchito zolimbitsa ukhondo.
Bungwe la WaterAid likugwira ntchito zake zolimbikitsa ukhondo osamba m’manja ku Nangalamu m’dera la mfumu yaikulu Bwananyambi komanso kwa Senior Chief Nankumba m’boma la Mangochi.