Bungwe la MEJN la chilimika pa ntchito yolimbikitsa maganizo am’gwiro pakati pa achinyamata m’boma la Mangochi.

Bungwe la Malawi Economic Justice Network MEJN lati ndi lodzipereka pa ntchito yolimbikitsa maganizo am’gwiro (Mental Health pachingerezi) pakati pa achinyamata m’dera la Monkey-bay m’boma la Mangochi.

A Tamanda Tembo, omwe ndi m’khalapakati wa bungwe la MEJN m’boma la Mangochi, ndi omwe anena izi lamulungu, 14 March 2026 pa mkumano omwe bungweli linachititsa ndi achinyamatawa pa sukulu ya pulayimale ya Monkeybay m’bomali omwe cholinga chake chinali chofuna kumva mavuto omwe achinyamata m’derali akukumana nawo pa nkhani ya malingaliro am’gwiro malinga ndi ufulu wachibadwidwe omwe achinyamatawa alinawo.

Mwa zina bungwe la MEJN lapeza kuti boma la Mangochi lili patsogolo pa nkhani zokhudza mavuto a malingaliro am’gwiro pakati pa achinyamata pomwe zadziwikanso kuti mavutowa akudza kaamba koti achinyamata ambiri m’bomali akuchita mchitidwe ogwiritsa ntchito makhwala ozunguza bongo komanso kumwa mowa mwa uchidakwa.

Poyankhula pa zokambiranazi, Favour Koloko yemwe ndi ophunzira wa standard 7 pa sukulu ya pulayimale ya Chitsanzo wati boma likuyenera kuwunikiranso ndi kukhwimitsa malamulo okhudza kugulitsa komanso kugwiritsa ntchito mankhwala ozunguza bongo ponena kuti malamulo omwe alipo pano sakugwiritsigwa ntchito moyenera.

Bungwe la MEJN likugwira ntchito ngati yomweyi pansi pa ntchito yotchedwa FORUT m’madera a mafumu akuluakulu anayi a Nankumba, Mponda, Chimwala ndi Jalasi m’boma la Mangochi.

Image from: https://www.holy-cross.com

Related posts

Dodma ili tcheru ngati madzi angasefukire

Ntchito za Climate Just Communities Zayenda Bwino

MANGOCHI SIKUCHITA BWINO PA NKHANI YOSAMBA M’MANJA