Bwalo loweruza milandu la Mangochi First Grade Magistrate lapeza a Steven Ajasi a zaka 45 olakwa ndikuwalipiritsa chindapusa cha ndalama zokwana K800, 000 kamba kopezeka ndi mafuta a galimoto ama litres 520 popanda chilolezo.
Pa 23 mwezi uno a Ajasi anawamanga atawapeza ndi mafuta a ndalama za nkhani-nkhani pa Roadblock ya Idrusi pamene anali pa ulendo ochokera ku Mangochi pa boma kupita ku Chiponde border.
Ku bwalo la milandu a Ajasi kudzera mwa owayimira pa milandu Counsel Smart Khalifa avomera mulanduwu popanda kukakamizadwa ndipo anapempha kuwachitira chifundo ponena kuti ataya ndalama zochuluka komanso ali ndi banja zomwe oyimira boma pa milandu Sub Inspector Davie Katandika watsutsa ponena kuti m’chitidwewu ukuyika miyoyo ya anthu ndi katundu pachiopsezo.
Mu chigamulo chake First Grade Magistrate Roy Kakutu wagwirizana ndi mbali ya boma polipiritsa a Ajasi chindapusachi ndikuti ngati atalephera akagwire ukaidi wakalavula gaga ku ndende kwa miyezi 8 ndipo walamulanso kuti mafutawo aperekedwe ku boma.
Pakadali pano a Ajasi omwe ndi a m’mudzi wa Nanyumbu kwa mfumu yaikulu Kawinga m’boma la Machinga alipira kale theka la chindapusachi pomwe theka linalo akuti apereka sabata ziwiri zisanathe.
(Wolemba : Micheal Kabuwe)