Home Business Nsewu wabwino ndi msanamira ya chitukuko-Jooma

Nsewu wabwino ndi msanamira ya chitukuko-Jooma

by Peter Dziyende
0 comments

Ngati njira imodzi yofuna kuchepetsa ngozi  mu nseu wa Mangochi-Monkey-bay, phungu wa dera la Monkey bay, a Ralph Jooma ayamba ntchito yokonza nseu-wu yomwe ndi ya ndalama zokwana pafupifupi 2 million kwacha.

Poyankhula ndi a Jooma, iwo ati kupatula kuchititsa ngozi, kuonongeka kwa nsewu wa Mangochi-Monkeybay kwakhala kukubweretsa mavuto osiyanasiyana  monga kukwera mtengo kwa maulendo a pa nseu,  kubwerela m’mbuyo kwa ntchito zokopa alendo, komanso kuonongeka kwa katundu monga nsomba zisanafike pa nsika kaamba kochedwa pa nseuwu.

Iwo anati akhala akupereka madando a vuto la kuonongeka kwa nseuwu ku  boma m’nyumba ya malamulo koma mpaka pano sanalandirebe yankho.

Nseuwu umalumikiza madera monga Mangochi boma, Golomoti komanso Monkey bay pa ntchito za malonda, zokopa alendo ndi zina .

You may also like

Leave a Comment

Dzimwe Community Radio is nonprofit making institution currently located behind the Community Resource Centre Hall to the South East of Monkey Bay Airstrip. The radio was established in 1998 initially funded by UNITED NATION EDUCATION SCIENTIFIC AND CULTURE ORGANISATION (UNESCO) to act as a platform where people can discuss issues and find lasting solutions that concern them to achieve sustainable development.

Newsletter

Subscribe my Newsletter for new blog posts, tips & new photos. Let's stay updated!

@2025 – All Right Reserved. MACRA Community Radios

Are you sure want to unlock this post?
Unlock left : 0
Are you sure want to cancel subscription?
-
00:00
00:00
Update Required Flash plugin
-
00:00
00:00